Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 1:15-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Pakuti, taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wacifumu wace pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa midzi yonse ya Yuda.

16. Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu yina, nagwadira nchito za manja ao.

17. Koma iwe ukwinde m'cuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.

18. Cifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mudzi walinga, mzati wacitsulo, makoma amkuwa, pa dziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akuru ace, ndi pa ansembe ace, ndi pa anthu a m'dziko.

19. Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; cifukwa Ine ndiri ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 1