Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Rute 1:6-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ace kuti abwerere kucoka m'dziko la Moabu; pakuti adamva m'dziko la Moabu kuti Yehova adasamalira anthu ace ndi kuwapatsa cakudya.

7. Naturuka iye kumene anakhalako ndi apongozi ace awiri pamodzi naye; namka ulendo wao kubwererakudzikola Yuda.

8. Ndipo Naomi anati kwa apongozi ace awiri, Mukani, bwererani yense wa inu ku nyumba ya amai wace; Yehova akucitireni zokoma, monga umo munacitira akufa aja ndi ine.

9. Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wace. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi.

10. Ndipo ananena naye, Iai, koma tidzapita nanu kwa anthu a kwanu.

11. Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? ngati ndiri nao m'mimba mwanga ana amuna ena kuti akhale amuna anu?

12. Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindikhoza kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndiri naco ciyembekezo, ndikakhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana amuna;

13. kodi mudzawalindirira akakula? mudzadziletsa osakwatibwa? Iai, ana anga, pakuti candiwawa koposa cifukwa ca inu popeza dzanja la Yehova landiturukira.

14. Nakweza iwo mau ao, naliranso misozi; ndi Olipa anampsompsona mpongozi wace, koma Rute anamkangamira.

15. Pamenepo anati, Taona mbale wako wabwerera kwa anthu a kwao, ndi kwa mulungu wace, bwerera umtsate mbale wako.

16. Nati Rute, Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga;

17. kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko; andilange Yehova naonjezeko, ciri conse cikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo.

18. Ndipo pakuona kuti analimbika kumuka naye, analeka kulankhula naye.

19. Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi?

20. Koma ananena nao, Musandicha Naomi, mundiehe Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandicitira zowawa ndithu.

21. Ndinacoka pane wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; mundicheranji Naomi, popeza Yehova wandicitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandicitira cowawa?

22. Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmoabu mpongozi wace pamodzi naye, amene anabwera kucokera ku dziko la Moabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kuceka barele.

Werengani mutu wathunthu Rute 1