Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 9:47-57 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

47. Ndipo anauza Abimeleki kuti amuna onse a nsanja ya ku Sekemu asonkhane.

48. Pamenepo Abimeleki anakwera kumka ku phiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m'dzanja lace Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kulika paphewa pace, nati kwa anthu okhala naye, Ici munaciona ndacita, fulumirani, mucite momwemo.

49. Ndi anthu onse anadulanso yense nthambi yace, natsata Abimeleki, naziika pangaka, natentha nazo ngakayo ndi moto; motero anthu onse a nsanja ya ku Sekemu anafanso, amuna ndi akazi ngati cikwi cimodzi.

50. Pamenepo Abimeleki anamuka ku Tebetsi, naumangira Tebetsi misasa, naulanda.

51. Koma m'mudzimo munali nsanja yolimba nathawira kumeneko amuna ndi akazi onse, ndi eni ace onse a mudziwo, nadzitsekereza m'mwemo, nakwera patsindwi pa nsanja.

52. Ndipo Abimeleki anafika kunsania, nalimbana nayo nkhondo, nayandikira kukhomo kwa nsanja, aitenthe ndi moto.

53. Ndipo mkazi wina anaponya mwana wa mphero pamutu pa Abimeleki, naphwanya bade lace.

54. Pamenepo anaitana msanga mnyamata wace wosenza zida zace, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wace, nafa iye.

55. Pamene amuna a Israyeli anaona kuti adafa Abimeleki anamuka yense kumalo kwace.

56. Momwemo Mulungu anambwezera Abimeleki coipaco anacitira atate wace ndi kuwapha abale ace makumi asanu ndi awiri.

57. Ndipo Mulungu anawabwezera coipa conse ca amuna a ku Sekemu pamitu pao, ndipo linawagwera temberero la Yotamu mwana wa Yerubaala.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 9