Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 9:17-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. pakuti atate wanga anakugwirirani nkhondo, nataya moyo wace, nakupulumutsani m'dzanja la Amidyani;

18. koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ace, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wace, akhale mfumu ya pa eni ace a ku Sekemu, cifukwa ali mbale wanu;

19. ngati tsono mwacitira Yerubaala ndi nyumba yace zoona ndi zangwiro lero lino, kondwerani naye Abimeleki, nayenso akondwere nanu;

20. koma ngati simunatero, uturuke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ace a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nuturuke mota kwa eni ace a ku Sekemu, ndi ku nyumba yace ya Milo, nunyeketse Abimeleki.

21. Pamenepo Yotamu anafulumira, nathawa, namuka ku Beeri, nakhala komweko, cifukwa ca Abimeleki mbale wace.

22. Abimeleki atakhala kalonga wa Israyeli zaka zitatu,

23. Mulungu anatumiza mzimu woipa pakati pa Abimeleki ndi eni ace a ku Sekemu; ndi eni ace a ku Sekemu anamcitira Abimeleki mosakhulupirika;

24. kuti ciwawa adacitira ana amuna makumi asanu ndi awiria Yerubaala cimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ace a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ace, awaphe abale ace.

25. Ndipo eni ace a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.

26. Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ace, napita ku Sekemu; ndi eni ace a ku Sekemu anamkhulupirira.

27. Ndipo anaturuka kumka kuminda, nachera mphesa m'mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m'nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki.

28. Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? sindiye mwana wa Yerubaala kodi? ndi Zebuli kazembe wace? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire cifukwa ninji?

29. Mwenzi anthu awa akadakhala m'dzanja langa; ndikadamcotsadi Abimeleki. Ndipo anati kwa Abimeleki, Curukitsa khamu lako, nuturuke.

30. Pamene Zebuli woyang'anira mudzi anamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, anapsa mtima.

31. Natuma mithenga kwa Abimeleki monyenga nati, Taonani Gaala ndi abale ace afika ku Sekemu; ndipo taonani, akupandukitsirani mudzi.

32. Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo;

33. ndipo kukhale kuti m'mawa, pakuturuka dzuwa, muuke mamawa mugwere mudziwo; ndipo taonani, akakuturukirani iye ndi anthu ali naye, uzimcitira monga lidziwa dzanja lako.

34. Pamenepo Abimeleki anauka ndi anthu onse anali naye, usiku; nalalira a ku Sekemu, magulu anai.

35. Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anaturuka, naima polowera pa cipata ca mudzi; nauka Abimeleki ndi anthu anali naye m'molalira.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 9