Ndipo tsopano, ngati mwacita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamcitira cokoma Yerubaala ndi nyumba yace, ndi kumcitira monga anayenera manja ace;