Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 9:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Abimeleki mwana wa Yerubaala anamuka ku Sekemu kwa abale a amai wace, nanena nao, ndi kwa banja lonse la nyumba ya atate wa amai wace, ndi kuti,

2. Nenanitu m'makutu mwa eni ace onse a ku Sekemu, Cokomera inu nciti, akulamulireni ana amuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? mukumbukilenso kuti ine ndine wa pfuko lanu ndi nyama yanu.

3. Pamenepo abale a amace anamnenera mau awa onse m'makutu a eni ace onse a Sekemu; ndi mitima yao inalunjika kutsata Abimeleki; pakuti anati, Ndiye mbale wathu.

4. Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pace ndi opepuka amene anamtsata.

5. Ndipo anamuka ku nyumba ya atate wace ku Ofira, nawapha abale ace ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.

6. Pamenepo anasonkhana eni ace onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa coimiritsa ciri m'Sekemu.

7. Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu pa phiri la Gerizimu, nakweza mau ace, napfuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ace a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 9