Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 14:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo ananena nao,Cakudya cinaturuka m'mwini kudya,Ndi cozuna cinaturuka m'mwini mphamvu,Ndipo masiku atatu sanakhoza kutanthauzira mwambiwo.

15. Koma kunali, tsiku lacisanu ndi ciwiri anati kwa mkazi wa Samsoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi mota. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo?

16. Ndipo mkazi wa Samsoni analira pamaso pace, nati, Ungondida, osandikonda; waphera anthu a mtundu wanga mwambi, osanditanthauzira ine. Ndipo ananena naye, Taona, sindinatanthauzira atate wanga kapena amai wanga, kodi ndikutanthauzire iwe?

17. Ndipo analira pamaso pace masiku asanu ndi awiriwo pocitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lacisanu ndi ciwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wace mwambiwo.

18. Ndipo amuna a pamudzi anati kwa Samsoni tsiku lacisanu ndi ciwiri, lisanalowe dzuwa, Cozuna coposa uci nciani; ndi camphamvu coposa mkango nciani? Pamenepo ananena nao,Mukadapanda kulima ndimthandi wanga,Simukadakumika mwambi wanga.

19. Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samsoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zobvala zao, nawapatsa okumika mwambiwo zobvala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kumka ku nyumba ya atate wace.

20. Ndipo mkazi wace wa Samsoni anakhala wa mnzace, amene adakhala bwenzi lace.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 14