Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 1:8-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo ana a Yuda anacita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi ndi moto.

9. Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwela ndi kucidikha.

10. Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala m'Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai.

11. Pocoka pamenepo anamuka kwa nzika za ku Dibiri, koma kale dzina la Dibiri ndilo mudzi wa Seferi.

12. Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha mudzi wa Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wace.

13. Ndipo Otiniyeli, mwana wa Kenazi mng'ono wa Kalebi anaulanda, ndipo anampatsa Akisa mwana wace wamkazi akhale mkazi wace.

14. Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkakamiza mwamuna wace kuti apemphe atate wace ampatse munda; natsika pa buru wace; ndipo Kalebe ananena naye, Ufunanji?

15. Ndipo anati kwa Iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko lakumwela, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi.

16. Ndipo ana a Mkeni mlamu wace wa Mose, anakwera kuturuka m'mudzi wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'cipululu ca Yuda cokhala kumwela kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.

17. Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkuru wace, nakantha Akanani akukhala m'Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mudziwo analicha Horima.

18. Yuda analandanso Gaza ndi malire ace, ndi Asikeloni ndi malire ace, ndi Ekroni ndi malire ace.

19. Ndipo Yehova anali ndi Yuda, iye nawaingitsa a kumapiri, osaingitsanzika za kucigwa, popeza zinali nao magareta acitsulo.

20. Ndipo anapatsa Kalebe Hebroni monga Mose adanena; iye nawaingitsa komweko ana amuna atatu a Anaki.

21. Koma ana a Benjamini sanaingitsa Ayebusi okhala m'Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala m'Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino.

22. Ndipo anakwera iwo a m'nyumba ya Yosefe naonso kumka ku Beteli; ndipo Yehova anakhala nao.

23. Ndipo iwo a m'nyumba ya Yosefe anatumiza ozonda ku Beteli. Koma kale dzina la mudziwo ndilo Luzi.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 1