Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 1:21-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Koma ana a Benjamini sanaingitsa Ayebusi okhala m'Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala m'Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino.

22. Ndipo anakwera iwo a m'nyumba ya Yosefe naonso kumka ku Beteli; ndipo Yehova anakhala nao.

23. Ndipo iwo a m'nyumba ya Yosefe anatumiza ozonda ku Beteli. Koma kale dzina la mudziwo ndilo Luzi.

24. Ndipo alonda anaona munthu alikuturuka m'mudzi, nanena naye, Utionetsetu nolowera m'mudzi, ndipo tidzakucitira cifundo.

25. Nawaonetsa polowera m'mudzi iye, naukantha mudzi iwowa ndi lupanga lakuthwa; koma analola munthuyo ndi banja lace lonse amuke.

26. Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mudzi, naucha dzina lace Luzi; ndilo dzina lace mpaka lero lino.

27. Koma Manase sanaingitsa a ku Betiseani ndi midzi yace kapena a Taanaki ndi midzi yace, kapena nzika za ku Dori ndi midzi yace, kapena nzika za ku Ibleamu ndi midzi yace, kapena nzika za ku Megido ndi midzi yace; koma Akanani anakhumba kukhala m'dziko muja.

28. Ndipo kunali, atakula mphamvu Israyeli, anasonkhetsa Akanani, osawaingitsa onse.

29. Ndipo Efraimu sanaingitsa Akanani okhala m'Gezeri; koma Akanani anakhala m'Gezeri pakati pao,

30. Zebuloni sanaingitsa nzika za ku Kitroni, kapena nzika za ku Nahaloli; koma Akanaru anakhala pakati pao, nawasonkhera.

31. Aseri sanaingitsa nzika za ku Ako, kapena nzika za ku Sidoni, kapena a Akalabu, kapena a Akisibu, kapena a Heliba, kapena a Afiki, kapena a Rehobo;

32. koma Aseri anakhala pakati pa Akanani nzika za kudziko; pakuti sanawaingitsa.

33. Nafitali sanaingitsa nzika za ku Beti-semesi, kapena nzika za ku Beri-anati; koma anakhala pakati pa Akanani, nzika za kudziko; koma nzika za ku Beti-semesi, ndi a ku Beti-anati zinawasonkhera.

34. Ndipo Aamori anakankha ana a Dani akhale kumapiri pakuti sanawalola atsikire kucigwa;

35. Aamori anakhumbanso kukhala ku phiri la Heresi, ku Ajaloni, ndi ku Saalibimu; koma dzanja la a m'nyumba ya Yosefe linawalaka, nakhala iwo akupereka msonkho.

36. Ndipo malire a Aamori anayambira pokwerera pa Akrabimu, pathanthwe, ndi pokwererapo.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 1