Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 1:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. NDIPO atafa Yoswa, ana a Israyeli anafunsira kwa Yehova ndi kuti, Adzayamba ndani kutikwerera pa Akanani kuwathira nkhondo?

2. Ndipo Yehova anati, Akwere Yuda; taonani, ndapereka dzikoli m'dzanja lace.

3. Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkuru wace, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.

4. Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m'dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi.

5. Ndipo anapeza Adoni-bezeki m'Bezeki, namthira nkhondo nakantha Akanani ndi Aperizi.

6. Koma Adoni-bezeki anathawa; ndipo anampitikitsa, namgwira, namdula zala zazikuru za m'manja ndi za m'mapazi.

7. Pamenepo anati Adoni-bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikuru za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinacita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.

8. Ndipo ana a Yuda anacita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi ndi moto.

9. Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwela ndi kucidikha.

10. Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala m'Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai.

11. Pocoka pamenepo anamuka kwa nzika za ku Dibiri, koma kale dzina la Dibiri ndilo mudzi wa Seferi.

12. Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha mudzi wa Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wace.

13. Ndipo Otiniyeli, mwana wa Kenazi mng'ono wa Kalebi anaulanda, ndipo anampatsa Akisa mwana wace wamkazi akhale mkazi wace.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 1