Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Obadiya 1:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. MASOMPHENYA a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yocokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.

2. Taona, ndakuika wamng'ono mwa amitundu; unyozedwa kwambiri.

3. Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwace, Adzanditsitsira pansi ndani?

4. Cinkana ukwera pamwamba peni peni ngati ciombankhanga, cinkana cisanja cako cisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.

5. Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akuchera mphesa sadzasiya khunkha kodi?

6. Ha! za Esau zasanthulidwa; ha! zobisika zace zafunidwa.

7. Anthu onse a akupangana nawe anakuperekeza mpaka pamalire; anthu okhala ndi mtendere nawe anakunyenga, nakuposa mphamvu; iwo akudya cakudya cako akuchera msampha pansi pako; mulibe nzeru mwa iye.

8. Ati Yehova, Kodi sindidzaononga tsiku lija anzeru mwa Edomu, ndi luntha m'phiri la Esau?

Werengani mutu wathunthu Obadiya 1