Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwenzi utakhala ngati mlongwanga,Woyamwa pa bere la amai!Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona;Osandinyoza munthu.

2. Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai,Kuti andilange mwambo; Ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa,Ndi madzi a makangaza anga.

3. Dzanja lamanzere lace akadanditsamiritsa kumutu,Lamanja lace ndi kundifungatira.

4. Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Muutsiranji, mugalamutsiranji cikondi,Cisanafune mwini.

5. Ndaniyu acokera kucipululu,Alikutsamira bwenzi lace?Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe:Pomwepo amako anali mkusauka nawe,Pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.

6. Undilembe pamtima pako, mokhoma cizindikilo, nundikhomenso cizindikilo pamkono pako;Pakuti cikondi cilimba ngati imfa;Njiru imangouma ngati manda:Kung'anima kwace ndi kung'anima kwa moto,Ngati mphezi ya Yehova,

7. Madzi ambiri sangazimitse cikondi,Ngakhale mitsinje yodzala kucikokolola:Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yace ngati sintho la cikondi,Akanyozedwa ndithu.

8. Tiri ndi mlongwathu wamng'ono,Alibe maere;Ticitirenji mlongwathuTsiku lokhoma unkhoswe wace?

9. Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva:Ngati ndiye citseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.

10. Ndine khoma, maere anga akunga nsanja zace:Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.

11. Solomo anali ndi munda wamipesa ku Baalahamoni;Nabwereka alimi mundawo;Yense ambwezere ndalama cikwi cifukwa ca zipatso zace.

12. Koma munda wanga wamipesa, uli pamaso panga ndiwo wangatu;Naco cikwico, Solomo iwe,Koma olima zipatso zace azilandira mazana awiri.

13. Namwaliwe wokhala m'minda,Anzake amvera mau ako:Nanenso undimvetse.

14. Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga,Dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawalaPa mapiri a mphoka,