Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 7:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ha, mapazi ako akongola m'zikwakwata,Mwana wamkaziwe wa mfumu!Pozinga m'cuuno mwako pakunga zonyezimira,Nchito ya manja a mmisiri waluso.

2. Pamcombo pako pakunga cikho coulungika,Cosasowamo vinyo wosanganika:Pamimba pako pakunga mulu wa tiriguWozingidwa ndi akakombo.

3. Maere ako akunga ana awiri a nswalaAnabadwa limodzi.

4. Khosi lako likunga nsanja yaminyanga;Maso ako akunga matawale a ku Hesiboni,A pa cipata ca Batirabimu;Mphuno yako ikunga nsanja ya ku LebanoImene iloza ku Damasiko.

5. Mutu wako ukunga Karimeli,Ndi tsitsi la pamtu pako likunga nsaru yakuda;Mfumu yamangidwa ndi nkhata zace ngati wamsinga.

6. Ha, ndiwe wokongola ndi wofunika,Bwenziwe, m'zokondweretsa!

7. Msinkhu wakowu ukunga mlaza,Maere ako akunga matsango amphesa,

8. Ndinati, Ndikakwera pamlazapo,Ndikagwira nthambi zace:Maere ako ange ngati matsango amphesa,Ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula;

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 7