Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 5:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndinamtsegulira bwenzi langalo;Koma ndinampeza, bwenzi langa atacoka.Moyo wanga unalefuka polankhula iye:Ndinamfunafuna, osampeza;Ndinamuitana, koma sanandibvomera.

7. Alonda akuyenda m'mudzi anandipeza,Nandikantha, nanditema;Osunga maguta nandicotsera cophimba canga.

8. Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza ciani?Kuti ndadwala ndi cikondi.

9. Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,Mkaziwe woposa kukongola?Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,Kuti utilumbirira motero?

10. Wokondedwa wanga ali woyera ndi wofiira,Womveka mwa zikwi khumi.

11. Mutu wace ukunga golidi, woyengetsa,Tsitsi lace lopotana, ndi lakuda ngati khungubwi.

12. Ana a maso ace akunga nkhunda pambali pa mitsinje ya madzi;Otsukidwa ndi mkaka, okhala pa mitsinje yodzala.

13. Masaya ace akunga citipula cabzyalamo ndiwo,Ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira:Milomo yace ikunga akakombo, pakukhapo madzi a nipa.

14. Manja ace akunga zing'anda zagolidi zoikamo zonyezimira zoti biriwiri:Thupi lace likunga copanga ca minyanga colemberapo masafiro.

15. Miyendo yace ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira,Zogwirika m'kamwa mwa golidi:Maonekedwe ace akunga Lebano, okometsetsa ngati mikungudza.

16. M'kamwa mwace muli mokoma: inde, ndiye wokondweretsa ndithu.Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa,Ana akazi inu a ku Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 5