Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 3:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Pali mphoyo, ndi nswala ya kuthengo,Kuti musautse, ngakhale kugalamutsa cikondi,Mpaka cikafuna mwini.

6. Ndaniyu akwera kuturuka m'cipululu ngati utsi wa tolo,Wonunkhira ndi nipa ndi mtanthanyerere,Ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?

7. Taonani, ndi macila a Solomo;Pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi,A mwa ngwazi za Israyeli.

8. Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo:Yense ali ndi lupanga lace pancafu pace,Cifukwa ca upandu wa usiku.

9. Solomo mfumu anadzipangira macila okhalamo tsongaNdi matabwa a ku Lebano.

10. Anapanga timilongoti tace ndi siliva,Ca pansi pace ndi golidi, mpando wace ndi nsaru yakuda,Pakati pace panayalidwa za cikondi ca ana akazi a ku Yerusalemu.

11. Turukani, ana akazi inu a Ziyoni, mupenye Solomo mfumu,Ndi korona amace anambveka naye tsiku la ukwati wace,Ngakhale tsiku lakukondwera mtima wace.

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 3