Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 2:11-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pakuti, taona, cisanu catha,Mvula yapita yaleka;

12. Maluwa aoneka pansi;Nthawi yoyimba mbalame yafika,Mau a njiwa namveka m'dziko lathu;

13. Mkuyu uchetsa nkhuyu zace zosakhwima,Mipesa niphuka,Inunkhira bwino.Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.

14. Nkhunda yangawe, yokhala m'ming'alu ya thanthwe, mobisika motsetsereka,Ndipenye nkhope yako, ndimve manako;Pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola.

15. Mutigwirire ankhandwe, ngakhale ang'ono, amene akuononga minda yamipesa;Pakuti m'minda yathu yamipesa muphuka biriwiri.

16. Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wace:Aweta zace pakati pa akakombo,

17. Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,Bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawalaPa mapiri a mipata.

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 2