1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2. Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali manu ndi ziwirizo ziwale pandunji pace pa coikapo nyalico.
3. Ndipo Aroni anacita cotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pace pa coikapo nyali, monga Yehova adauza Mose.
4. Ndipo mapangidwe ace a coikapo nyali ndiwo golidi wosula; kuyambira tsinde lace kufikira maluwa ace anacisula; monga mwa maonekedwe ace Yehova anaonetsa Mose, momwemo anacipanga coikapo nyali.
5. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
6. Uwatenge Alevi pakati pa ana a Israyeli, nuwayeretse.
7. Ndipo utere nao kuwayeretsa: uwawaze madzi akucotsa zoipa, ndipo apititse lumo pa thupi lao lonse, natsuke zobvala zao, nadziyeretse.
8. Pamenepo atenge ng'ombe yamphongo ndi nsembe yace yaufa, ufa wosanganiza ndi mafuta; utengenso ng'ombe yamphongo yina ikhale nsembe yaucimo.
9. Ndipo ubwere nao Alevi pakhomo pa cihema cokomanako; nuwasonkhanitse khamu lonse la ana a Israyeli;
10. nubwere nao Alevi pamaso pa Yehova; ndi ana a Israyeli aike manja ao pa Alevi;
11. ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yocokera kwa ana a Israyeli, kuti akhale akucita nchito ya Yehova,
12. Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yaucimo, ndi inzace, nsembe yopsereza za Yehova, kucita cotetezera Alevi.