Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 7:86-89 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

86. Zipande zagolidi ndizo khumi ndi ziwiri, zodzala ndi cofukiza, cipande conse masekeli khumi, kuyesa sekeli wa malo opatulika; golidi wonse wa zipandezo ndiwo masekeli zana limodzi ndi makumi awiri;

87. ng'ombe zonse za nsembe yopsereza ndizo ng'ombe khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziwiri, ana a nkhosa a caka cimodzi khumi ndi awiri, pamodzi ndi nsembe yao yaufa; ndi atonde a nsembe zaucimo khumi ndi awiri;

88. ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, ana a nkhosa a caka cimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka ciperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.

89. Ndipo polowa Mose ku cihema cokomanako, kunena ndi iye, anamva Mau akunena naye ocokera ku cotetezerapo ciri pa likasa la mboni, ocokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo iye ananena naye.

Werengani mutu wathunthu Numeri 7