Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 7:79-88 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

79. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

80. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

81. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

82. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

83. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ici ndi copereka ca Ahira mwana wa Enani.

84. Uku ndi kupereka ciperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israyeli, tsiku la kudzoza kwace: mbizi zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolidi khumi ndi ziwiri;

85. mbizi yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika.

86. Zipande zagolidi ndizo khumi ndi ziwiri, zodzala ndi cofukiza, cipande conse masekeli khumi, kuyesa sekeli wa malo opatulika; golidi wonse wa zipandezo ndiwo masekeli zana limodzi ndi makumi awiri;

87. ng'ombe zonse za nsembe yopsereza ndizo ng'ombe khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziwiri, ana a nkhosa a caka cimodzi khumi ndi awiri, pamodzi ndi nsembe yao yaufa; ndi atonde a nsembe zaucimo khumi ndi awiri;

88. ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, ana a nkhosa a caka cimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka ciperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.

Werengani mutu wathunthu Numeri 7