Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 7:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kumuutsa kacisi, namdzoza ndi kumpatula, ndi zipangizo zace zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zace zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;

2. akalonga a Israyeli, akuru a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mapfuko akuyang'anira owerengedwa;

3. anadza naco copereka cao pamaso pa Yehova, magareta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi ng'ombe khumi ndi ziwfri; akalonga awiri anapereka gareta mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa kacisi.

4. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

5. Uzilandira kwa iwo, kuti zikhale zakucitira nchito ya cihema cokomanako; nuzipereke kwa Alevi, yense monga mwa nchito yace.

6. Ndipo Mose analandira magareta ndi ng'ombe, nazipereka kwa Alevi.

7. Anapatsa ana a Gerisoni magareta awiri ndi ng'ombe zinai, monga mwa nchito yao;

8. napatsa ana a Merari magareta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa nchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe.

9. Koma sanapatsa ana a Kohati kanthu; popeza nchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao.

10. Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka ciperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera naco copereka cao pa guwa la nsembelo.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Akalonga onse, yense pa tsiku lace, apereke zopereka zao za kupereka ciperekere guwa la nsembe.

12. Wakubwera naco copereka cace tsiku loyamba ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu, wa pfuko la Yuda:

Werengani mutu wathunthu Numeri 7