Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 5:18-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Mulungu, nabvula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yacikumbutso m'manja mwace, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwace mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.

19. Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagona nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kucidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.

20. Koma iwe, ngati wapatukira mwamuna wako, ngati wadetsedwa, kuti wagona nawe munthu, wosati mwamuna wako;

21. pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'cuuno mwako, ndi kukutupitsa mbulu;

22. ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa mbulu ndi kuondetsa m'cuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.

23. Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.

24. Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira.

Werengani mutu wathunthu Numeri 5