Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 4:27-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Nchito yonse ya ana a Agerisoni, kunena za akatundu ao ndi nchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ace amuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.

28. Iyi ndi nchito ya mabanja a ana a Gerisoni m'cihema cokomanako; ndipo Itamara mwana wa Aroni wansembe ayang'anire udikiro wao.

29. Kunena za ana a Merari, Uwawerenge monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao.

30. Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kucita nchito ya cihema cokomanako.

31. Ndipo udikiro wa akatundu ao, monga mwa nchito zao zonse m'cihema cokomanako ndi ici: matabwa a kacisi, ndi mitanda yace, ndi mizati ndi nsanamira zace, ndi makamwa ace;

32. ndi nsici za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ace, ndi ziciri zace, ndi zingwe zace, pamodzi ndi zipangizo zace zonse, ndi nchito yace yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwaehula maina ao.

33. Iyi ndi nchito ya mabanja a ana a Merari, monga mwa nchito zao zonse m'cihema cokomanako, mowauza Itamara mwana wa Aroni wansembe.

34. Ndipo Mose ndi Aroni ndi akalonga a khamu anawerenga ana a Akohati monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao,

35. kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire Debito m'cihema cokomanako;

36. ndipo owerengedwa ao monga mwa mabanja ao ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.

37. Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'cihema cokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 4