Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 4:24-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Nchito ya mabanja a Agerisoni, pogwira nchito ndi kusenza katundu ndi iyi;

25. azinyamula nsaru zophimba za kacisi, ndi cihema cokomanako, cophimba cace, ndi cophimba ca zikopa za akatumbu ciri pamwamba pace, ndi nsaru yotsekera pa khomo la cihema cokomanako;

26. ndi nsaru zocingira za pabwalo, ndi nsaru yotsekera ku cipata ca pabwalo liri pakacisi ndi pa guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za Debito zao, ndi zonse acita nazo; m'menemo muli nchito zao.

27. Nchito yonse ya ana a Agerisoni, kunena za akatundu ao ndi nchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ace amuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.

28. Iyi ndi nchito ya mabanja a ana a Gerisoni m'cihema cokomanako; ndipo Itamara mwana wa Aroni wansembe ayang'anire udikiro wao.

29. Kunena za ana a Merari, Uwawerenge monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao.

30. Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kucita nchito ya cihema cokomanako.

31. Ndipo udikiro wa akatundu ao, monga mwa nchito zao zonse m'cihema cokomanako ndi ici: matabwa a kacisi, ndi mitanda yace, ndi mizati ndi nsanamira zace, ndi makamwa ace;

32. ndi nsici za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ace, ndi ziciri zace, ndi zingwe zace, pamodzi ndi zipangizo zace zonse, ndi nchito yace yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwaehula maina ao.

33. Iyi ndi nchito ya mabanja a ana a Merari, monga mwa nchito zao zonse m'cihema cokomanako, mowauza Itamara mwana wa Aroni wansembe.

34. Ndipo Mose ndi Aroni ndi akalonga a khamu anawerenga ana a Akohati monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao,

35. kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire Debito m'cihema cokomanako;

36. ndipo owerengedwa ao monga mwa mabanja ao ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.

37. Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'cihema cokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.

38. Ndipo ana owerengedwa a Gerisoni, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyu mba za makolo ao,

Werengani mutu wathunthu Numeri 4