Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 4:1-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2. Werengani ana a Kohati pakati pa ana a Levi, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao,

3. kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire nchito ya cihema cokomanako.

4. Nchito ya ana a Kohati m'cihema cokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulikitsa:

5. akati amuke a m'cigono, Aroni ndi ana ace amuna azilowa, natsitse nsaru yocinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni,

6. ndi kuikapo cophimba ca zikopa za akatumbu; ndi kuyalapo nsaru yamadzi yeni yeni, ndi kupisako mphiko zace.

7. Ndi pa gome la mkate waonekera ayale nsaru yamadzi, naikepo mbale zace, ndi zipande, ndi mitsuko, ndi zikho zakuthira nazo; mkate wa cikhalire uzikhalaponso.

8. Ndipo ayale pa izi nsaru yofiira, ndi kuliphimba ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zace.

9. Ndipo atenge nsaru yamadzi, ndi kuphimba coikapo nyali younikira, ndi nyali zace, ndi mbano zace, ndi zaolera zace, ndi zotengera zace zonse za mafuta zogwira nazo nchito yace.

10. Ndipo acimange ndi cipangizo zace zonse m'cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa conyamulira.

11. Ndipo pa guwa la nsembe lagolidi aziyala nsaru yamadzi, naliphimbe ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zace.

12. Natenge zipangizo zace zonse za utumiki, zimene atumikira nazo m'malo opatulika, nazimange m'nsaru yamadzi, ndi kuziphimba ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kuziika paconyamulira.

13. Ndipo azicotsa mapulusa pa guwa la nsembe, ndi kuyala pa ilo nsaru yofiirira.

14. Naikepo zipangizo zace zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zaolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zace.

15. Atatha Aroni ndi ana ace amuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zace zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'cigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'cihema cokomanako.

16. Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi cofukiza ca pfungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa kacisi wonse, ndi zonse ziri m'mwemo, malo opatulika, ndi zipangizo zace.

17. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Dati,

18. Musamasadza pfuko la mabanja a Kohati kuwacotsa pakati pa Alevi;

Werengani mutu wathunthu Numeri 4