Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 36:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo pofika caka coliza ca ana a Israyeli adzaphatikiza colowa cao ku colowa ca pfuko limene akhalako; cotero adzacotsa colowa cao ku colowa ca pfuko la makolo athu.

5. Ndipo Mose analamulira ana a Israyeli monga mwa mau a Yehova, nati, Pfuko la ana a Yosefe linena zaona.

6. Colamulira Yehova za ana akazi a Tselofekadi ndi ici, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ace; komatu akwatibwe nao a banja la pfuko la makolo ao okha okha.

7. Motero colowa ca ana a Israyeli sicidzamka m'pfuko m'pfuko; popeza ana a Israyeli adzamamatira yense ku colowa ca pfuko la makolo ace.

8. Ndipo mwana wamkazi yense wa mapfuko a ana a Israyeli, wakukhala naco colowa, akwatibwe ndi wina wa banja la pfuko la kholo lace, kuti ana a Israyeli akhale naco yense colowa ca makolo ace.

9. Motero colowa ca ana a Israyeli sicidzamka m'pfuko m'pfuko, pakuti mapfuko a ana a Israyeli adzamamatira lonse ku colowa cace cace.

10. Monga Yehova adalamulira Mose, momwemo ana akazi a Tselofekadi anacita;

11. popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana akazi a Tselofekadi, anakwatibwa ndi ana amuna a abale a atate wao.

12. Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo colowa cao dnakhala m'pfuko la banja la atate wao.

13. Awa ndi malamulo ndi maweruzo, amene Yehova analamulira ana a Israyeli ndi dzanja la Mose m'zidikha za Moabu pa Yordano ku Yeriko.

Werengani mutu wathunthu Numeri 36