Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 36:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo akakwatibwa nao ana amuna a mapfuko ena a ana a Israyeli, acicotse colowa cao ku colowa ca makolo athu, nacionjeze ku colowa ca pfuko limene adzakhalako; cotero acicotse ku maere a colowa cathu.

4. Ndipo pofika caka coliza ca ana a Israyeli adzaphatikiza colowa cao ku colowa ca pfuko limene akhalako; cotero adzacotsa colowa cao ku colowa ca pfuko la makolo athu.

5. Ndipo Mose analamulira ana a Israyeli monga mwa mau a Yehova, nati, Pfuko la ana a Yosefe linena zaona.

6. Colamulira Yehova za ana akazi a Tselofekadi ndi ici, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ace; komatu akwatibwe nao a banja la pfuko la makolo ao okha okha.

7. Motero colowa ca ana a Israyeli sicidzamka m'pfuko m'pfuko; popeza ana a Israyeli adzamamatira yense ku colowa ca pfuko la makolo ace.

8. Ndipo mwana wamkazi yense wa mapfuko a ana a Israyeli, wakukhala naco colowa, akwatibwe ndi wina wa banja la pfuko la kholo lace, kuti ana a Israyeli akhale naco yense colowa ca makolo ace.

9. Motero colowa ca ana a Israyeli sicidzamka m'pfuko m'pfuko, pakuti mapfuko a ana a Israyeli adzamamatira lonse ku colowa cace cace.

Werengani mutu wathunthu Numeri 36