Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 36:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo akuru a makolo a mabanja a ana a Gileadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, wa mabanja a ana a Yosefe, anayandikiza, nanena pamaso pa Mose, ndi pamaso pa akalonga, ndiwo akuru a makolo a ana a Israyeli;

2. nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israyeli dzikoli mocita maere likhale colowa cao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ace akazi colowa ca Tselofekadi mbale wathu.

3. Ndipo akakwatibwa nao ana amuna a mapfuko ena a ana a Israyeli, acicotse colowa cao ku colowa ca makolo athu, nacionjeze ku colowa ca pfuko limene adzakhalako; cotero acicotse ku maere a colowa cathu.

4. Ndipo pofika caka coliza ca ana a Israyeli adzaphatikiza colowa cao ku colowa ca pfuko limene akhalako; cotero adzacotsa colowa cao ku colowa ca pfuko la makolo athu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 36