4. ndi malire anu adzapinda kucokera kumwela kumka pokwera Akrabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kuturuka kwace adzacokera kumwela ku Kadesi Barinea, nadzaturuka kumka ku Hazara Adara, ndi kupita kumka ku Azimoni;
5. ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kumka ku mtsinje wa Aigupto, ndi kuturuka kwao adzaturuka kunyanja.
6. Kunena za malire a kumadzulo, nyanja yaikuru ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo.
7. Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku nyanja yaikuru mulinge ku phiri la Hori:
8. kucokera ku phiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kuturuka kwace kwa malire kudzakhala ku Zedadi.
9. Ndipo malirewo adzaturuka kumka ku Zifironi, ndi kuturuka kwace kudzakhala ku Hazara Enani; ndiwo malire anu a kumpoto.
10. Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ocokera ku Hazara Enani kumka ku Sefamu;
11. ndi malire adzatsika ku Sefamu kumka ku Ribala, kum'mawa kwa Ayina; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,
12. ndi malire adzatsika ku Yordano, ndi kuturuka kwace kudzakhala ku Nyanja ya Mcere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ace polizinga.
13. Ndipo Mose anauza ana a Israyeli, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kucita maere, limene Yehova analamulira awapatse mapfuko asanu ndi anai ndi hafu;
14. popeza pfuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi pfuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi pfuko la hafu la Manase lalandira colowa cao;
15. mapfuko awiriwa ndi hafu adalandira colowa cao tsidya lija la Yordano ku Yeriko, kum'mawa, koturukira dzuwa.