Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Malire a dziko la Kanani

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2. Uza ana Israyeli, nunene nao, Mutalowa a m'dziko la Kanani, ndilo dziko logwera inu, likhale colowa canu, dziko ija Kanani monga mwa malire ace,

3. dera lanu la kumwela lidzakhala locokera ku cipululu ca Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwela adzakhala ocokera ku malekezero a Nyanja ya Mcere kum'mawa;

4. ndi malire anu adzapinda kucokera kumwela kumka pokwera Akrabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kuturuka kwace adzacokera kumwela ku Kadesi Barinea, nadzaturuka kumka ku Hazara Adara, ndi kupita kumka ku Azimoni;

5. ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kumka ku mtsinje wa Aigupto, ndi kuturuka kwao adzaturuka kunyanja.

6. Kunena za malire a kumadzulo, nyanja yaikuru ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo.

7. Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku nyanja yaikuru mulinge ku phiri la Hori:

8. kucokera ku phiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kuturuka kwace kwa malire kudzakhala ku Zedadi.

9. Ndipo malirewo adzaturuka kumka ku Zifironi, ndi kuturuka kwace kudzakhala ku Hazara Enani; ndiwo malire anu a kumpoto.

10. Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ocokera ku Hazara Enani kumka ku Sefamu;

11. ndi malire adzatsika ku Sefamu kumka ku Ribala, kum'mawa kwa Ayina; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa,

12. ndi malire adzatsika ku Yordano, ndi kuturuka kwace kudzakhala ku Nyanja ya Mcere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ace polizinga.

13. Ndipo Mose anauza ana a Israyeli, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kucita maere, limene Yehova analamulira awapatse mapfuko asanu ndi anai ndi hafu;

14. popeza pfuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi pfuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi pfuko la hafu la Manase lalandira colowa cao;

15. mapfuko awiriwa ndi hafu adalandira colowa cao tsidya lija la Yordano ku Yeriko, kum'mawa, koturukira dzuwa.

16. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

17. Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale colowa canu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni.

18. Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku pfuko limodzi, agawe dziko likhale colowa cao.

19. Maina a amunawo ndiwo: wa pfuko la Yuda, Kalebi mwana wa Yefune.

20. Wa pfuko la ana a Simeoni, Semuyeli mwana wa Amihudi.

21. Wa pfuko la Benjamini, Elidadi mwana wa Kisiloni.

22. Wa pfuko la ana a Dani, kalonga Buki mwana wa Yogili.

23. Wa ana a Yosefe; wa pfuko la ana a Manase, kalonga Haniyeli mwana wa Efodi.

24. Wa pfuko la ana a Efraimu, kalonga Kemuyeli mwana wa Sipitana.

25. Wa pfuko la ana a Zebuloni, kalonga Elisafana mwana wa Paranaki.

26. Wa pfuko la ana a Isakara, kalonga Palitiyeli mwana wa Azana.

27. Wa pfuko la ana a Aseri, kalonga Ahihudi mwana wa Selomi.

28. Wa pfuko la ana a Nafitali, kalonga Pedaheli mwana wa Amihudi.

29. Iwo ndiwo amene Yehova analamulira agawire ana a Israyeli colowa cao m'dziko la Kanani.