3. dera lanu la kumwela lidzakhala locokera ku cipululu ca Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwela adzakhala ocokera ku malekezero a Nyanja ya Mcere kum'mawa;
4. ndi malire anu adzapinda kucokera kumwela kumka pokwera Akrabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kuturuka kwace adzacokera kumwela ku Kadesi Barinea, nadzaturuka kumka ku Hazara Adara, ndi kupita kumka ku Azimoni;
5. ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kumka ku mtsinje wa Aigupto, ndi kuturuka kwao adzaturuka kunyanja.
6. Kunena za malire a kumadzulo, nyanja yaikuru ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo.
7. Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku nyanja yaikuru mulinge ku phiri la Hori:
8. kucokera ku phiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kuturuka kwace kwa malire kudzakhala ku Zedadi.