Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 33:36-54 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Nacokera ku Ezioni Geberi, nayenda namanga m'cipululu ca Zini (ndiko Kadesi).

37. Nacokera ku Kadesi, nayenda namanga m'phiri la Hori, ku malekezero a dziko la Edomu.

38. Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto zaka makumi anai, mwezi wacisanu, tsiku loyamba la mwezi.

39. Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori.

40. Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwela m'dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israyeli.

41. Ndipo anacokera ku phiri la Hori, nayenda namanga m'Tsalimona.

42. Nacokera ku Tsalimona, nayenda namanga m'Punoni.

43. Nacokera ku Punoni, nayenda namanga m'Oboti.

44. Nacokera ku Oboti, nayenda namanga m'iye Abarimu, m'malire a Moabu.

45. Nacokera ku lyimu, nayenda namanga m'Diboni Gadi.

46. Nacokera ku Diboni Gadi, nayenda namanga m'Alimoni Diblataimu.

47. Nacokera ku Alimoni Diblataimu, nayenda namanga m'mapiri a Abarimu, cakuno ca Nebo.

48. Nacokera ku mapiri a Abarimu, nayenda namanga m'zidikhaza Moabu pa Yordano ku Yeriko,

49. Ndipo anamanga pa Yordano, kuyambira ku Beti Yesimoti kufikira ku Abeli Sitimu m'zidikha za Moabu.

50. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Moabu pa YordaBaku Yeriko, nati,

51. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutaoloka Yordano kulowa m'dziko la Kanani,

52. mupitikitse onse okhala m'dzikopamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;

53. ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanu lanu.

54. Ndipo mulandire dzikoli ndi kucita maere monga mwa mabanja anu; colowa cao cicurukire ocurukawo, colowa cao cicepere ocepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwace; mulandire colowa canu monga mwa mapfuko a makolo anu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 33