Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 32:5-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale lao lao; tisaoloke Yordano.

6. Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno?

7. Ndipo mufoketseranji mtima wa ana a Israyeli kuti asaoloke ndi kulowa dzikoli Yehova anawapatsa?

8. Anatero makolo anu, muja ndinawatumiza acoke ku Kadesi Barinea kukaona dziko.

9. Popeza atakwera kumka ku cigwa ca Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israyeli, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa.

10. Ndipo Yehova anapsa mtima tsiku lija, nalumbira iye, nati,

11. Anthu adakwerawo kuturuka m'Aigupto, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo; popeza sananditsata Ine ndi mtima wonse;

12. koma Kalebi mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse.

13. Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israyeli, nawayendetsa-yendetsa m'cipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udacita coipa pamaso pa Yehova.

14. Ndipo taonani, mwauka m'malo mwa makolo anu, gulu la anthu ocimwa, kuonjezanso mkwiyo waukali wa Yehova pa Israyeli,

15. Pakuti mukabwerera m'mbuyo kusamtsata iye, adzawasiyanso m'cipululu, ndipo mudzaononga anthu awa onse.

16. Ndipo anayandikiza, nati, Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu midzi; koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israyeli, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao;

17. ndi ang'ono athu adzakhala m'midzi ya malinga cifukwa ca okhala m'dzikomo.

18. Sitidzabwerera kwathu, kufikira ana a Israyeli atalandira yense colowa cace.

19. Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordano, ndi m'tsogolo mwace; popeza colowa cathu tacilandira tsidya lino la Yordano kum'mawa.

20. Ndipo Mose anati nao, Ngati mudzacita ici, ndi kudzikonza kunkhondo pamaso pa Yehova,

21. ndi kuoloka Yordano pamaso pa Yehova okonzeka onse mwa inu, kufikira atapitikitsa adani ace pamaso pace,

Werengani mutu wathunthu Numeri 32