Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 32:32-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

32. Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma colowa cathu cathu cikhale tsidya lino la Yordano.

33. Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi pfuko la hafu la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basana, dzikoli ndi midzi yace m'malire mwao, ndiyo midzi ya dziko lozungulirako,

34. Ndipo ana a Gadi anamanga Diboni, ndi Ataroti, ndi Aroeri;

35. Ataroti Sofani, Yazeri, ndi Yogebeha;

36. ndi Beti Nimira, ndi Beti Harani: midzi ya m'malinga, ndi makola a zoweta.

37. Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyali, ndi Kiriyataimu;

38. ndi Nebo, ndi Baala Meoni (nasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaicha midzi adaimanga ndi maina ena.

39. Ndipo ana a Makiri mwana wa Manase anamka ku Gileadi, naulanda, napitikitsa Aamori anali m'mwemo.

40. Ndipo Mose anapatsa Makiri mwana wa Manase Gileadi; ndipo anakhala m'menemo.

41. Ndipo Yairi mwana wa Manase anamka nalanda midzi yao, naicha Havoti Yairi. Ndipo Noba anamka nalanda Kenati, ndi miraga yace, naucha Noba, dzina lace.

Werengani mutu wathunthu Numeri 32