Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 32:28-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akuru a makolo a mapfuko a ana a Israyeli za iwo.

29. Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordano, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Gileadi likhale lao lao;

30. koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko ao ao pakati pa inu m'dziko la Kanani.

31. Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzacita.

32. Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma colowa cathu cathu cikhale tsidya lino la Yordano.

33. Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi pfuko la hafu la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basana, dzikoli ndi midzi yace m'malire mwao, ndiyo midzi ya dziko lozungulirako,

34. Ndipo ana a Gadi anamanga Diboni, ndi Ataroti, ndi Aroeri;

35. Ataroti Sofani, Yazeri, ndi Yogebeha;

36. ndi Beti Nimira, ndi Beti Harani: midzi ya m'malinga, ndi makola a zoweta.

37. Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyali, ndi Kiriyataimu;

Werengani mutu wathunthu Numeri 32