Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 32:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma ana a Rubeni ndi ana a Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazeri, ndi dziko la Gileadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.

2. Pamenepo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anadza nanena ndi Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga a khamulo, nati,

3. Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazeri, ndi Nimra, ndi Heseboni, ndi Eleyali, ndi Sebamu, ndi Nebo, ndi Beoni,

4. dzikoli Yehova analikantha pamaso pa khamu la Israyeli, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta.

5. Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale lao lao; tisaoloke Yordano.

6. Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno?

7. Ndipo mufoketseranji mtima wa ana a Israyeli kuti asaoloke ndi kulowa dzikoli Yehova anawapatsa?

8. Anatero makolo anu, muja ndinawatumiza acoke ku Kadesi Barinea kukaona dziko.

9. Popeza atakwera kumka ku cigwa ca Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israyeli, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa.

10. Ndipo Yehova anapsa mtima tsiku lija, nalumbira iye, nati,

11. Anthu adakwerawo kuturuka m'Aigupto, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo; popeza sananditsata Ine ndi mtima wonse;

12. koma Kalebi mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse.

13. Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israyeli, nawayendetsa-yendetsa m'cipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udacita coipa pamaso pa Yehova.

14. Ndipo taonani, mwauka m'malo mwa makolo anu, gulu la anthu ocimwa, kuonjezanso mkwiyo waukali wa Yehova pa Israyeli,

15. Pakuti mukabwerera m'mbuyo kusamtsata iye, adzawasiyanso m'cipululu, ndipo mudzaononga anthu awa onse.

16. Ndipo anayandikiza, nati, Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu midzi; koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israyeli, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao;

Werengani mutu wathunthu Numeri 32