Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 31:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo anawathira nkhondo Amidyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse.

8. Ndipo anapha mafumu a Amidyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekamu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.

9. Ndipo ana a Israyeli anagwira akazi a Amidyani, ndi ana ang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi cuma cao conse.

10. Ndipo anatentha ndi moto midzi yao yonse yokhalamo iwo, ndi zigono zao zonse.

11. Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama.

12. Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israyeli, kucigono, ku zidikha za Moabu, ziri ku Yordano pafupi pa Yeriko.

13. Ndipo Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga onse a khamulo, anaturuka kukomana nao kunja kwa cigono.

14. Ndipo Mose anakwiya nao akazembe a nkhondoyi, atsogoleri a zikwi, atsogoleri a mazana, akufuma kunkhondo adaithira.

15. Ndipo Mose ananena nao, Kodi mwasunga ndi moyo akazi onse?

16. Taonani, awa analakwitsa ana a Israyeli pa Yehova nilica Peoricija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova.

Werengani mutu wathunthu Numeri 31