Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israyeli, kucigono, ku zidikha za Moabu, ziri ku Yordano pafupi pa Yeriko.