Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 31:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Mose anawatuma a pfuko limodzi cikwi cimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Pinehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lace.

7. Ndipo anawathira nkhondo Amidyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse.

8. Ndipo anapha mafumu a Amidyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekamu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.

9. Ndipo ana a Israyeli anagwira akazi a Amidyani, ndi ana ang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi cuma cao conse.

10. Ndipo anatentha ndi moto midzi yao yonse yokhalamo iwo, ndi zigono zao zonse.

11. Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama.

12. Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israyeli, kucigono, ku zidikha za Moabu, ziri ku Yordano pafupi pa Yeriko.

Werengani mutu wathunthu Numeri 31