Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 31:38-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ndipo ng'ombe zidafikira zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri.

39. Ndipo aburu anafikira zikwi makumi atatu ndi mazana asanu; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi limodzi mphambu mmodzi.

40. Ndipo anthu anafikira zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo anthu makumi atatu mphambu awiri.

41. Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.

42. Ndipo kunena za gawo la ana a Israyeli, limene Mose adalicotsa kwa anthu ocita nkhondowo,

43. (ndipo gawo la khamulo ndilo nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu,

44. ndi ng'ombe zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi,

45. ndi aburu zikwi makumi atatu ndi mazana asanu,

46. ndi anthu zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi,)

47. mwa gawolo la ana a Israyeli Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa kacisi wa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

48. Pamenepo akazembe a pa ankhondo zikwi, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, anayandikiza kwa Mose;

49. nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowa munthu mmodzi wa ife.

50. Ndipo tabwera naco copereka ca Yehova, yense cimene anacipeza, zokometsera zagolidi, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kucita cotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.

51. Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golidiyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka.

52. Ndipo golidi yense wa nsembe yokweza ya Yehova amene anapereka kwa Yehova, wofuma kwa atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo masekeli zikwi khumi ndi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu.

53. Popeza wankhondo yense anadzifunkhira yekha.

Werengani mutu wathunthu Numeri 31