Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 31:17-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo tsono iphani amuna onse mwa anawo, iphaninso akazi onse akudziwa mwamuna mogona naye.

18. Koma ana akazi onse osadziwa mwamuna mogona naye, asungeru ndi moyo akhale anu.

19. Ndipo mukhale m'misasa kunja kwa cigono masiku asanu ndi awiri; ali yense adapha munthu, ndi ali yense wakukhudza wophedwa, mudziyeretse tsiku lacitatu ndi lacisanu ndi ciwiri, inu ndi andende anu.

20. Muyeretse zobvala zanu zonse, zipangizo zonse zacikopa, ndi zaomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse zamtengo.

21. Ndipo Eleazara wansembe ananena ndi ankhondo adapita kunkhondowo, Lemba la cilamuloco Yehova analamulira Mose ndi ili:

22. Golidi, ndi siliva, mkuwa, citsulo, ndolo ndi mtobvu zokha,

23. zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi.

24. Ndipo muzitsuke zobvala zanu tsiku lacisanu ndi ciwiri, kuti mukhale oyera; ndipo mutatero mulowe m'cigono.

25. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

26. Werengani zakunkhondo, ndizo anthu, ndi zoweta, iwe; ndi Eleazara wansembe, ndi akuru a nyumba za makolo za khamulo;

27. nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anaturuka kunkhondo, ndi khamu lonse.

28. Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akuturuka kunkhondo apereke kwa Yehova; munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa aburu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.

29. Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.

30. Ndipo ku gawo la ana a Israyeli utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa aburu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa kacisi wa Yehova.

31. Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe anacita monga Yehova anamuuza Mose.

32. Ndipo zakunkhondo, zotsalira zofunkha zonse adazifunkha ankhondowa, ndizo nkhosa zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zikwi makumi asanu ndi awiri kudza zisanu,

Werengani mutu wathunthu Numeri 31