1. Ndipo Mose ananena ndi akuru a mapfuko a ana a Israyeli, nati, Cinthu anacilamulira Yehova ndi ici:
2. Munthu akacitira Yehovacowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wace codziletsa, asaipse mau ace; azicita monga mwa zonse zoturuka m'kamwa mwace.
3. Ndipo mkazi akacitira Yehova cowinda, nakadzimanga naco codziletsa, pokhala ali m'nyumba ya atate wace, m'unamwali;
4. ndipo atate wace akamva cowinda cace, ndi codziletsa cace anamanga moyo wace naco, koma wakhala naye cete atate wace; pamenepo zowinda zace zonse zidzakhazikika, ndi codziletsa ciri: conse wamanga naco moyo wace cidzakhazikika.
5. Koma atate wace akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zace zonse, ndi zodziletsa zace zonse anamanga nazo moyo wace, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wace anamletsa.
6. Ndipo akakwatibwa naye mwamuna, pokhala ali nazo zowinda zace, kapena zonena zopanda pace za milomo yace, zimene anamanga nazo moyo wace;
7. nakazimva mwamuna wace, nakakhala naye cete tsiku lakuzimva iye; pamenepo zowinda zace zidzakhazikika, ndi zodziletsa anamanga nazo moyo wace zidzakhazikika.
8. Kama mwamuna wace akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza cowinda cace anali naco, ndi zonena zopanda pace za milomo yace, zimene anamanga nazo moyo wace; ndipo Yehova adzamkhululukira.
9. Koma cowinda ca mkazi wamasiye, kapena mkazi wocotsedwa, ziti zonse anamanga nazo moyo wace zidzamkhazikikira.