Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 3:29-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Mabanja a ana a Kohati azimanga mahema ao pa mbali ya kacisi ya kumwera.

30. Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafana mwana wa Uziyeli.

31. Ndipoudikirowaondiwo likasa, ndi gome, ndi coikapo nyali, ndimagome a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene acita nazo, ndi nsaru yocinga, ndi nchito zace zonse.

32. Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pa malo opatulika.

33. Banja la Amali, ndi banja la Amusi ndiwo a Merari; ndiwo mabanja a Merari.

34. Ndipo owerengedwa ao, powerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi zisanu ndi cimodzi kudza mazana awiri.

35. Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja a Merari ndiye Zuriyeli mwana wa Abiyaili; azimanga mahema ao pa mbali ya kacisi ya kumpoto.

36. Ndipo coyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a kacisi, ndi mitanda yace, ndi mizati ndi nsanamira zace, ndi makamwa ace, ndi zipangizo zace zonse, ndi nchito zace zonse;

37. ndi nsici za pabwalo pozungulira, ndi makamwa ace, ndi ziciri zace, ndi zingwe zace.

38. Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la kacisi, kum'mawa, pa khomo la cihema cokomanako koturukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ace amuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israyeli; koma mlendo wakuyandikizako amuphe,

39. Owerengedwa onse a Alevi, adawawerenga Mose ndi Aroni, powauza Yehova, monga mwa mabanja ao, amuna onse kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.

Werengani mutu wathunthu Numeri 3