Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 28:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo dzuwa la Sabata ana a nkhosa awiri a caka cimodzi, opanda cirema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi nsembe yace yothira;

10. ndiyo nsembe yopsereza ya dzuwa la Sabata liri lonse, pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yothira.

11. Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi opanda cirema;

12. ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa ng'ombe iri yonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo;

13. ndi limodzi la magawo khumi la ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndiwo wa mwana wa nkhosa yense; ndiyo nsembe yopsereza ya pfungo lokoma, nsembe yamoto ya. Yehova.

14. Ndipo nsembe zace zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la bini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwana wa nkhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uli wonse kunena miyezi yonse ya caka.

15. Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yaucimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yothira.

16. Ndipo mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi, pali paskha wa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Numeri 28