Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 27:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo anayandikiza ana akazi a Tselofekadi mwana wa Heferi, ndiye mwana wa Gileadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ace akazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.

2. Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga, ndi khamu lonse, pakhomo pa cihema cokomanako, ndi kuti,

3. Atate wathu adamwalira m'cipululu, ndipo sanakhala iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zace zace; ndipo analibe ana amuna.

4. Licotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lace, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathu lathu pakati pa abale a atate wathu.

5. Ndipo Mose anapita nao mlandu wao pamaso pa Yehova.

6. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

Werengani mutu wathunthu Numeri 27