Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 26:30-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Ana a Gileadi ndiwo: Yezeri, ndiye kholo la banja la Ayezeri; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki;

31. ndi Asiriyeli, ndiye kholo la banja la Aasiriyeli; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu;

32. ndi Semida, ndiye kholo la banja la Asemida; ndi Heferi, ndiye kholo la banja la Aheferi.

33. Ndipo Tselofekadi mwana wa Heferi analibe ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana akazi a Tselofekadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.

34. Iwo ndiwo mabanja ao a Manase; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

35. Ana amuna a Efraimu monga mwa mabanja ao ndiwo: Sutela, ndiye kholo la banja la Asutela; Bekeri, ndiye kholo la banja la Abekeri; Tahana, ndiye kholo la banja la Atahana.

Werengani mutu wathunthu Numeri 26