Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 26:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ana amuna a Gadi monga mwa mabanja ao ndiwo: Zefoni, ndiye kholo la banja la Azefoni; Hagi, ndiye kholo la banja la Ahagi; Suni, ndiye kholo la banja la Asuni;

16. Ozini, ndiye kholo la banja la Aozini; Eri, ndiye kholo la banja la Aeri;

17. Arodi, ndiye kholo la banja la Aarodi; Areli, ndiye kholo la banja la Aareli.

18. Iwo ndiwo mabanja a ana a Gadi, monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi anai ndi mazana asanu.

19. Ana amuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani.

20. Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.

21. Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezeroni, ndiye kholo la banja la Ahezeroni; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli.

22. Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi kudza mazana asanu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 26