Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 23:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Pamenepo Mulungu anakomana ndi Balamu; ndipo ananena ndi iye, Ndakonza maguwa a nsembe asanu ndi awiri, ndipo ndapereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe liri lonse.

5. Ndipo Yehova anaika mau m'kamwa mwa Balamu, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene cakuti cakuti.

6. Ndipo anabwerera kwa iye, ndipo, taonani, analikuima pa nsembe yopsereza yace, iye ndi akalonga onse a Moabu.

7. Ndipo ananena fanizo lace, nati,Ku Aramu ananditenga Balaki,Mfumu ya Moabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa;Idza, udzanditembererere Yakobo.Idza, nudzanyoze Israyeli.

8. Ndidzatemberera bwanji amene Mulungu sanamtemberera?Ndidzanyoza bwanji, amene Yehova sanamnyoza?

9. Pakuti, pokhala pamwamba pa matanthwe ndimpenya,Pokhala pa zitunda ndimuyang'ana;Taonani, ndiwo anthu akukhala paokha.Osadziwerengera pakati pa amitundu ena,

10. Adzawerenga ndani pfumbi la Yakobo,Kapena kuwerenga limodzi la magawo anai la Israyeli?Ndipo ine ndife monga amafa aongoka mtima,Citsiriziro canga cifanane naco cace!

11. Pamenepo Balaki anati kwa Balamu, Wandicitiranji? Ndinakutenga utemberere adani anga, ndipo taona, wawadalitsa ndithu.

12. Ndipo anayankha nati, Cimene aciika m'kamwa mwanga Yehova, sindiyenera kodi kunena ici?

13. Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.

Werengani mutu wathunthu Numeri 23