Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 21:18-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Citsime adakumba mafumu,Adacikonza omveka a anthu;Atanena mlamuli, ndi ndodo zao.Ndipo atacoka kucipululu anamuka ku Matana;

19. atacoka ku Matana ku Nahaliyeli; atacoka ku Nahaliyeli ku Bamoti;

20. atacoka ku Bamoti ku cigwa ciri m'dziko la Moabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndicipululu.

21. Ndipo Israyeli anatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ndi kuti,

22. Ndipitire pakati pa dziko lako; sitidzapatuka kulowa m'munda, kapena m'munda wampesa, sitidzamwako madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wacifumu, kufikira tapitirira malire ako.

23. Ndipo Sihoni sanalola Israyeli apitire m'malire ace; koma Sihoni anamemeza anthu ace onse, nadzakomana naye Israyeli m'cipululu, nafika ku Jahazi, nathira nkhondo pa Israyeli.

24. Ndipo Israyeli anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lace likhale lao lao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana ai Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba.

25. Ndipo Israyeli analanda midzi iyi yonse; nakhala Israyeli m'midzi yonse ya Aamori; m'Hesiboni ndi miraga yace yonse.

26. Popeza Hesiboni ndiwo mudzi wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Moabu, nilanda dziko lace m'dzanja lace kufikira Arinoni.

27. Cifukwa cace iwo akunena mophiphiritsa akuti,Idzani ku Hesiboni,Mudzi wa Sihoni umangike, nukhazikike:

28. Popeza moto unaturuka m'Hesiboni,Cirangali ca mota m'mudzi wa Sihoni;Catha Ari wa Moabu,Eni misanje ya Arinoni.

29. Tsoka kwa iwe, Moabu!Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu,Anapereka ana ace amuna opulumuka,Ndi ana ace akazi akhale ansinga,Kwa Sihoni mfumu ya Aamori.

30. Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni,Ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa,Ndiwo wakufikira ku Medeba.

31. Comweco Israyeli anakhala m'dziko la Aamori.

32. Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda miraga yace, napitikitsa Aamori a komweko.

Werengani mutu wathunthu Numeri 21