mbale zofukizazo za iwo amene adacimwira moyo wao wao, ndipo azisule zaphanthiphanthi, zikhale cibvundikilo ca guwa la nsembe; popeza anabwera nazo pamaso pa Yehova, cifukwa cace zikhala zopatulika; ndipo zidzakhala cizindikilo kwa ana a Israyeli.