Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 16:13-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. kodi ndi cinthu cacing'ono kuti watikweza kuticotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, kutipha m'cipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?

14. Ndiponso sunatilowetsa m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, kapena kutipatsa colowa ca minda, ndi minda yamphesa; kodi udzakolowola amuna awa maso ao? Sitifikako.

15. Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira copereka cao; siodinalanda buru wao mmodzi, kapena kucitira coipa mmodzi wa iwowa.

16. Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni;

17. nimutenge munthu yense mbale yace yofukizamo, nimuike cofukiza m'mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yace yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yace yofukizamo.

18. Potero munthu yense anatenga mbale yace yofukizamo, naikamo moto, naikapo cofukiza, naima pa khomo la cihema cokomanako pamodzi ndi Mose ndi Aroni.

19. Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la cihema cokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.

20. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

21. Dzipatu, leni pakati pa khamu lino, kuti ndi wathe m'kamphindi.

22. Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?

23. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

24. Nena ndi khamulo, ndi kuti, Kwerani kucoka pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu.

25. Ndipo Mose anauka namuka kwa Datani ndi Abiramu; ndi akuru a Israyeli anamtsata.

26. Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Cokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kali konse, mungaonongeke m'zocimwa zao zonse.

27. Potero anakwera kucokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anaturuka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna, ndi makanda ao.

28. Ndipo Mose anati, Ndi ici mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kucita nchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m'mtima mwanga mwanga.

29. Akafa anthu awa monga amafa anthu onse, kapena akasungika monga amasungika anthu onse, Yehova sananditumiza ine.

Werengani mutu wathunthu Numeri 16